•   Call Us: +265 1 756 000
  •   muscco@muscco.org

Features

Membala Opambana: BANJA LA BAMBO NDI MAI CHINANGWA PDF

Jun 20 2016

Pamene mabanja ambili akulephela kutukuka chifukwa cha kusamvana pakati pa bambo ndi mayi m’banjamo, ku Thyolo mu dela la Namsanya, banja lina la chitsanzo likusimba lokoma. Banjali lomwe ndi la bambo ndi mai Chinangwa, ndipo lili ndi ana atatu, limagwilila ntchito limodzi momvana , mokondana ndi mogonjelana ndipo izi zathandiza kuti pakhomo pawo pakhale pa mwana alirenji. Bambo Francis Ladison Chinangwa amachokela mu mudzi wa Chimwanya, mfumu yayikulu Namseta mu boma la thyolo ndipo mayi Triza Chinangwa amachokelaso mu boma lomwelo la thyolo koma m’mudzi wa Namsanya, mfumu yayikulu Mchilamwela. Mayi Chinangwa amagwila ntchito ya uphunzitsi pa sukulu ya Namsanya ndipo amuna awo ndi munthu wa bizinesi. Chozizwitsa ndi chakuti onsewa ndi mamembala a Thyolo Teachers SACCO yomwe ndi SACCO ya aphunzitsi mu bomalo.

“Anayamba kulowa SACCO ndi akazi anga mu chaka cha 1996 ndipo nthawi imeneyo ndinali ndikupanga ntchito ya umpalamatabwa pamene iwowa amaphunzitsa pa sukulu ya Mikombe”, anayamba choncho kufotokoza zambili ya banjali bambo chinangwa. “pokopeka ndi mpata wa ngongole yofewa omwe amaupeza mayiwa ku SACCO, ndinawalimbikitsa kuti asunge umwini wambili mpaka titapeza mpamba oyamba bizinezi yayikulu”. Mu chaka cha 2005, bambo Chinangwa anapanga chiganizo cholowa nawo SACCO ndi lingalilo lotengela limodzi ngongole ndi akazi awo kuti ayambe bizinezi ya kumtima kwawo. “Nthawi imeneyo ndinali nditafunsa ku SACCO ngati angavomele amuna anga kukhala nawo gawo la SACCOyi”, adatelo mayi Chinangwa. Chaka chomwecho anatenga ngongole yawo yoyamba yomwe anagwilitsa ntchito pogulila malo komanso kuyambila bizinezi ya grocery. Kuchokela mu bizinezi ya grocery imeneyi, lero banja la a Chinangwa lili ndi magalimoto awili oyendela, nyumba ya makono komanso akupanga ulimi wa nkhuku ndi nkhumba. “Titayamba bizinezi ya grocery, sitinasiye za umpalamatabwa. Tinabweza ngongole mofulumila ku SACCO ndikupezanso ina yomwe tinagwilitsa ntchito pomangila nyumba”. Lero lino banjali linamanga nyumba ya zipinda zinayi, balaza, podyela komanso yokhala ndi zimbudzi mkati. Mbali ina ya nyumbayi, anatsekulako grocery ndipo ndiyimene mai Chinangwa amayiyang’anila akaweluka ku sukulu. Iwo, monyadila, anati sakhala pa renti ndipo sadankhawa zothamangitsidwa m’nyumba chifukwa cha kuchepekedwa kwa makobidi. SACCO ya Thyolo Teachers idawathandizanso ndi mpamba woyambila ulimi woweta nkhuku za chakudya mu chaka cha 2008. Kupyolera mu ulimiwu, banjali limagulitsa nkhuku zosachepela 500 masabata awili ali wonse. Pamodzi banjali lili ndi nkhuku zosachepela 1000. “pambali pa nkhukuzi, tilinso ndi nkhumba khumi ndi ziwili (12) koma zinalipo makumi awili ndi zisanu (25). Zinazo tagulitsa posachedwa”, anatelo bambo Chinangwa akusekelela. “chifukwa cha SACCO, takwanitsanso kugula magalimoto awili ndipo onsewa timawabweleketsa ku anthu powalipitsa kangachepe”. Mu chaka cha 2011 banjali linakatenga ngongole yochulukilapo ku SACCO yomwe anagulila galimoto la makono yotchedwa Toyota Platz. Banjali lakwanitsa kumanganso manyumba ena awili omwe anayikamo anthu a lendi ndipo mwezi ndi mwezi amakhala akutolela ndalama. Potsendela kucheza kwathu, bambo ndi mayi Chinangwa analimbikitsa mabanja mu dziko lino kuti aphunzile kudalilana ndi kugwilila ntchito limodzi pakuti ichi ndiye chiyambi cha kupambana mu moyo.

Read 133566 times
Rate this item
(2 votes)

About The Author